Deuteronomy 19:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Musamchitire chifundo. Mchotseni pakati pa Aisraele munthu wopha mnzake wosalakwa, kuti zinthu zikuyendereni bwino.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Diso lanu lisamchitire chifundo, koma muchotse mwazi wosachimwa m'Israele, kuti chikukomereni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Osamumvera chisoni. Muyenera kuchotsa tchimo lokhetsa magazi wosalakwa mu Israeli kuti zinthu zizikuyenderani bwino.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Diso lanu lisamcitire cifundo, koma mucotse mwazi wosacimwa m'Israyeli, kuti cikukomereni.