Deuteronomy 19:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
M'choloŵa chomwe mudzakhala mutalandira m'dziko limene Chauta, Mulungu wanu, akukupatsanilo, musakaŵafutuze malire a mnzanu amene anthu akale adakhazika.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Musamasendeza malire a mnansi wanu, amene adawaika iwo a kale lomwe, m'cholowa chanu mudzalandirachi, m'dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani likhale lanulanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Musamasunthe mwala wa malire anu ndi mnzanu amene anayikidwa ndi makolo anu pa cholowa chimene mulandire mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Musamasendeza malire a mnansi wanu, amene adawaika iwo a kale lomwe, m'colowa canu mudzalandiraci, m'dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani likhale lanu lanu.