Deuteronomy 19:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mboni imodzi sikwanira kumtsimikiza munthu kuti wachimwadi kapena kuti wapalamuladi mlandu pakuchita cholakwa chakutichakuti. Chofunika nchakuti pakhale mboni ziŵiri kapena zitatu zotsimikiza kuti munthuyo walakwadi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mboni imodzi isamaukira munthu pa mphulupulu iliyonse, kapena tchimo lililonse adalichimwa; pakamwa pa mboni ziwiri, kapena pakamwa pa mboni zitatu mlandu utsimikizike.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mboni imodzi siyokwanira kupeza munthu kuti ndi wolakwa pa mlandu uliwonse umene wapalamula. Nkhani itsimikizike ndi umboni wa anthu awiri kapena atatu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mboni imodzi isamaukira munthu pa mphulupulu iri yonse, kapena cimo liri lonse adalicimwa; pakamwa pa mboni ziwiri, kapena pakamwa pa mboni zitatu mlandu utsimikizike.