Deuteronomy 19:20 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono wina aliyense akadzamva zimene zachitika, adzakhala ndi mantha, ndipo palibe ndi mmodzi yemwe mwa inu amene adzachitenso choipa choterechi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo otsalawo adzamva, nadzaopa, ndi kusachitanso monga choipacho pakati panu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu ena onse adzamva zimenezi nachita mantha, ndipo choyipa choterechi sichidzachitikanso pakati panu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo otsalawo adzamva, nadzaopa, ndi kusacitanso monga coipaco pakati panu.