Deuteronomy 19:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nali lamulo lokhalira munthu wopha mnzake, amene angapulumutse moyo wake pothaŵira kumeneko: Munthu akapha mnzake mwangozi, osati chifukwa cha chidani, athaŵire ku mzinda uliwonse mwa mizinda imeneyo kuti apulumuke.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mlandu wa munthu wakupha mnzake wakuthawirako nakhala ndi moyo ndiwo: wakupha mnzake osati dala, osamuda kale lonse;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ili ndi lamulo lokhudza munthu amene wapha mnzake mosazindikira osati mwadala, nathawira kumeneko kupulumutsa moyo wake. Ndi munthu amene wapha mnzake mosazindikira, popanda maganizo oyipa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mlandu wa munthu wakupha mnzace wakuthawirako nakhala ndi moyo ndiwo: wakupha mnzace osati dala, osamuda kale lonse;