Deuteronomy 19:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mwachitsanzo, anthu aŵiri apita ku thengo limodzi kukadula mitengo. Wina podula mtengo, nkhwangwa nkuguluka, nipha mnzakeyo. Iye angathe kuthaŵira ku umodzi mwa mizinda imeneyi, napulumuka.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
monga ngati munthu analowa kunkhalango ndi mnzake kutema mitengo, ndi dzanja lake liyendetsa nkhwangwa kutema mtengo, ndi nkhwangwa iguluka m'mpinimo, nikomana ndi mnzake, nafa nayo; athawire ku wina wa midzi iyi, kuti akhale ndi moyo;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mwachitsanzo, munthu atapita ku nkhalango ndi mnzake kukadula mitengo, ndiye posamula nkhwangwa kuti adule mtengo, nkhwangwa ikhoza kuguluka nʼkukagwera mnzake uja nʼkumupha. Munthu ameneyo akhoza kuthawira ku umodzi mwa mizindayo napulumutsa moyo wake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
monga ngati munthu analowa kunkhalango ndi mnzace kutema mitengo, ndi dzanja lace liyendetsa nkhwangwa kutema mtengo, ndi nkhwangwa iguruka m'mpinimo, nikomana ndi mnzace, nafa nayo; athawire ku wina wa midzi iyi, kuti akhale ndi moyo;