Deuteronomy 19:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Akapanda kutero, mwina chifukwa cha kutalika kwa mtunda, wachibale wofuna kumlipsira adzamthamangira mwaukali, nkumugwira wothaŵayo namupha, ngakhale ali wosayenera kuphedwa, chifukwa paja popha munthu mwangozi analibe chidani chilichonse ndi amene adafayo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
kuti wolipsa mwazi angalondole wakupha mnzake, pokhala mtima wake watentha, nampeza, popeza njira njaitali, namkantha kuti wafa; angakhale sanapalamule imfa, poona sanamude kale lonse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kupanda kutero ndiye kuti wolipsira akhoza kumuthamangitsa mwaukali ndi kumugwira ngati mtunda utalika, ndipo akhoza kumupha ngakhale kuti sanayenera kufa popeza sanaphe mnzake mwadala.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
kuti wolipsa mwazi angalondole wakupha mnzace, pokhala mtima wace watentha, nampeza, popeza njira njaitali, namkantha kuti wafa; angakhale sanaparamula imfa, poona sanamuda kale lonse.