Deuteronomy 19:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
pamenepo mudzapatulenso mizinda ina itatu. Adzakuwonjezerani dziko ndithu, malinga mukamakachita zonse zimene ndikukulamulani, ndiye kuti kukonda Chauta, Mulungu wanu, ndi kuchita zonse zimene akukuphunzitsani.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ukadzasunga lamulo ili lonse kulichita, limene ndikuuzani lero lino, kukonda Yehova Mulungu wanu, ndi kuyenda m'njira zake masiku onse; pamenepo mudzionjezere midzi itatu ina pamodzi ndi itatu iyi;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
chifukwa chotsatira bwino malamulo onse amene ndikukuwuzani lero, kukonda Yehova Mulungu wanu ndi kuyenda mʼnjira zake nthawi zonse, ndiye kuti mukuyenera kupatula mizinda itatu yowonjezera.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ukadzasunga lamulo ili lonse kulicita, limene ndikuuzani lero lino, kukonda Yehova Mulungu wanu, ndi kuyenda m'njira zace masiku onse; pamenepo mudzionjezere midzi itatu yina pamodzi ndi itatu iyi;