Deuteronomy 2:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tidabwerera kupita ku chipululu podzera njira ya ku Nyanja Yofiira, monga momwe Chauta adatilamulira. Ndipo tidakhala tikuzungulira phiri la Seiri masiku ambiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo tinabwerera, ndi kuyenda kunka kuchipululu, kutsata njira ya Nyanja Yofiira, monga Yehova adanena ndi ine; ndipo tinapaza phiri la Seiri masiku ambiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka tinabwerera ndi kuyamba ulendo wolowera ku chipululu motsatira njira ya ku Nyanja Yofiira, monga mmene Yehova anatilamulira. Kwa nthawi yayitali tinayendayenda cha ku dziko la mapiri la Seiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo tinabwerera, ndi kuyenda kumka kucipululu, kutsata njira ya Nyanja Yofiira, monga Yehova adanena ndi ine; ndipo tinapaza phiri la Seiri masiku ambiri.