Deuteronomy 2:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ahorinso ankakhala ku Seiri, koma zidzukulu za Esau zidaŵapirikitsa, ndi kuwononga mtundu wonse. Atatero, iwo adakhala ku dziko la Seiri. Adachita zimenezi monga momwe Aisraele adapirikitsira adani ao m'dziko limene Chauta adaŵapatsa.)
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Ahori anakhala m'Seiri kale, koma ana a Esau analanda dziko lao, nawaononga pamaso pao, nakhala m'malo mwao; monga Israele anachitira dziko lakelake, limene Yehova anampatsa).
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ahori amakhala ku Seiri koma adzukulu a Esau anawapirikitsa. Iwo anawononga Ahori pamaso pawo nawakhalira pamalo pawo monga Aisraeli anachitira mʼdziko limene Yehova anawapatsa ngati chuma chawo).
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Ahori anakhala m'Seiri kale, koma ana a Esau analanda dziko lao, nawaononga pamaso pao, nakhala m'malo mwao; monga Israyeli anacitira dziko lace lace, limene Yehova anampatsa.)