Deuteronomy 2:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nthaŵi imene tidaoloka mtsinje wa Zerediwo, nkuti patapita kale zaka 38 kuyambira pamene tidakhala ku Kadesi-Baranea. Amuna odziŵa kumenya nkhondo nkuti atafa onse, monga momwe adaanenera Chauta molumbira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo masiku amene tinayenda kuchokera ku Kadesi-Baranea, kufikira tidaoloka mtsinje wa Zeredi, ndiwo zaka makumi atatu mphambu zisanu ndi zitatu; kufikira utatha mbadwo wonse wa amuna ankhondo m'chigono, monga Yehova adawalumbirira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Panapita zaka 38 kuchokera pa nthawi imene tinachoka ku Kadesi Barinea mpaka pamene tinawoloka Chigwa cha Zeredi. Pa nthawi imeneyi nʼkuti mʼbado wonse wa anthu ankhondowo utawonongeka ku msasa monga Yehova anawalumbirira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo masiku amene tinayenda kucokera ku Kadesi Barinea, kufikira tidaoloka mtsinje wa Zeredi, ndiwo zaka makumi atatu mphambu zisanu ndi zitatu; kufikira utatha mbadwo wonse wa amuna ankhondo m'cigono, monga Yehova adawalumbirira.