Deuteronomy 2:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono mukadzafika pafupi ndi dziko la Aamoni, musaŵavute kapena kuchita nawo nkhondo, chifukwa sindikupatsani dziko lao, popeza kuti dzikolo ndidalipereka kwa zidzukulu za Loti, kuti likhale laolao.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pamene uyandikiza popenyana ndi ana a Amoni, usawavuta, kapena kuutsana nao; popeza sindidzakupatsako dziko la ana a Amoni likhale lakolako; popeza ndinapatsa ana a Loti ili likhale laolao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mukafika kwa Aamoni, musawavutitse kapena kuwaputa, popeza sindidzakupatsani gawo lililonse la dziko la Aamoni. Ine ndalipereka dzikoli ngati chuma kwa adzukulu a Loti.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pamene uyandikiza popenyana ndi ana a Amoni, usawabvuta, kapena kuutsana nao; popeza sindidzakupatsako dziko la ana a Amoni likhale lako lako; popeza ndinapatsa ana a Loti ili likhale lao lao.