Deuteronomy 2:21 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kutalika kwao ankalingana ndi Aanaki. Anali anthu otchuka ndiponso ochuluka kwambiri. Komabe Chauta adaŵaononga, ndipo dziko lao lidatengedwa ndi Aamoni amene adakhazikika kumeneko.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndiwo anthu akulu, ndi ambiri, ndi atalitali, monga Aanaki; koma Yehova anawaononga pamaso pao; ndipo analanda dziko lao, nakhala m'malo mwao;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo anali anthu amphamvu ndiponso ochuluka, ataliatali ngati Aanaki. Yehova anawawononga ndi kuwachotsa pamaso pa Aamoni, amene anawapirikitsa nawakhalira pa malo pawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndiwo anthu akuru, ndi ambiri, ndi atalitali, monga Aanaki; koma Yehova anawaononga pamaso pao; ndipo analanda dziko lao, nakhala m'malo mwao;