Deuteronomy 2:22 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zimenezi ndi zomwe Chauta adaachita ndi zidzukulu za Esau zimene zinkakhala ku Seiri. Iye adaononga Ahori, ndipo dziko lao lidatengedwa ndi ana a Esauwo, nakhazikika kumeneko, ndipo akukhalako mpaka lero lino.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
monga Iye anachitira ana a Esau, akukhala m'Seiri, pamene anaononga Ahori pamaso pao; ndipo analanda dziko lao, nakhala m'malo mwao kufikira lero lomwe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova anachitanso chimodzimodzi ndi adzukulu a Esau omwe anakhazikika ku Seiri atawononga Ahori powachotsa pamaso pawo. Iwo anawapirikitsa Ahoriwo ndi kuwakhalira pamalo pawo mpaka lero.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
monga iye anacitira ana a Bsau, akukhala m'Seiri, pamene anaononga Ahori pamaso pao; ndipo analanda dziko lao, nakhala m'malo mwao kufikira lero lomwe.