Deuteronomy 2:24 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Chauta adaonjeza kuti, “Nyamukani tsopano, tiyeni, muwoloke mtsinje wa Arinoni. Ndikukupatsani Sihoni Mwamoriyo, mfumu ya Hesiboni, pamodzi ndi dziko lake lomwe. Mputeni, ndipo muyambepo kumenyana naye nkhondo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Uka, yenda ulendo wako, ndi kuoloka mtsinje wa Arinoni; taonani, ndapereka Sihoni mfumu ya Hesiboni, Mwamori, ndi dziko lake m'dzanja lako; yamba kulilandira, ndi kuutsana naye nkhondo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Tsopano nyamukani, muwoloke khwawa la Arinoni. Taona ndapereka mʼmanja mwako Sihoni Mwamori mfumu ya Hesiboni ndi dziko lake lonse. Yambapo kutenga chuma chake ndi kumenyana naye nkhondo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Uka, yenda ulendo wako, ndi kuoloka mtsinje wa Arinoni; taonani, ndapereka Sihoni mfumu ya Hesiboni, M-amori, ndi dziko lace m'dzanja lako; yamba kulilandira, ndi kuutsana naye nkhondo.