Deuteronomy 2:25 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndiyamba lero kuŵachititsa mantha anthu a pa dziko lapansi kuti azikuwopani. Aliyense akangomva za inu, adzanjenjemera ndi mantha ndi kuda nkhaŵa chifukwa choopa inu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tsiku lino ndiyamba kuopsetsa nawe ndi kuchititsa mantha nawe anthu a pansi pa thambo lonse, amene adzamva mbiri yako, nadzanjenjemera, nadzawawidwa chifukwa cha iwe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Lero lomwe lino ndidzayamba kuyika chiopsezo ndi mantha pa mitundu yonse pansi pa thambo kuti akuope. Iwowo adzamva zambiri yako ndipo adzanjenjemera ndi kuwawidwa mtima chifukwa cha iwe.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tsiku lino ndiyamba kuopsetsa nawe ndi kucititsa mantha nawe anthu a pansi pa thambo lonse, amene adzamva mbiri yako, nadzanjenjemera, nadzawawidwa cifukwa ca iwe.