Deuteronomy 2:26 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono ndidatuma amithenga kuchokera ku chipululu cha Kedemoti, kuti apite kwa mfumu Sihoni wa ku Hesiboni. Poŵatumapo, ndidaŵauza kuti akanene mau amtendere, kuti,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndinatuma amithenga ochokera ku chipululu cha Kedemoti kwa Sihoni mfumu ya Hesiboni ndi mau a mtendere, ndi kuti,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ine ndinatuma amithenga kuchokera ku chipululu cha Kedemoti kupita kwa Sihoni mfumu ya Hesiboni kukanena mawu ofuna mtendere ndipo ndinati,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndinatuma amithenga ocokera ku cipululu ca Kedemoti kwa Sihoni mfumu ya Hesiboni ndi mau a mtendere, ndi kuti,