Deuteronomy 2:30 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma mfumu Sihoni yekha sadatilole kuti tidzere m'dziko mwake. Chauta, Mulungu wanu, adamuumitsa khosi nampatsa mtima wouma, kuti ampereke m'manja mwathu monga momwe mukuwonera lero lino.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Sihoni mfumu ya Hesiboni sanatilole kupitira kwao; popeza Yehova Mulungu wanu anaumitsa mzimu wake, nalimbitsa mtima wake, kuti ampereke m'dzanja lanu, monga lero lino.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Sihoni mfumu ya Hesiboni sanalole kuti tidutse. Popeza Yehova Mulungu wanu analimbitsa mzimu wake, nawumitsa mtima wake kuti amupereke mʼmanja mwanu monga wachitira lero lino.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Sihoni mfumu ya Hesiboni sanatilola kupitira kwao; popeza Yehova Mulungu wanu anaumitsa mzimu wace, nalimbitsa mtima wace, kuti ampereke m'dzanja lanu, monga lero lino.