Deuteronomy 2:31 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Chauta adandiwuza kuti, “Taona ndayamba kale kukupatsa mfumu Sihoni ndi dziko lake lomwe. Uyambe kulilandadi, kuti mukakhale ndithu m'menemo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yehova anati kwa ine, Taona, ndayamba kupereka Sihoni ndi dziko lake pamaso pako; yamba kulandira dziko lake likhale lakolako.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova anati kwa ine, “Taona ndayamba kumupereka Sihoni ndi dziko lake kwa iwe. Tsopano yamba kugonjetsa ndi kulanda dziko lake.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yehova anati kwa ine, Taona, ndayamba kupereka Sihoni ndi dziko lace pamaso pako; yamba kulandira dziko lace likhale lako lako.