Deuteronomy 2:36 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kuchokera ku Aroere, mzinda umene uli pamphepete pa mtsinje wa Arinoni, ndiponso kuchokera ku mzinda umene uli m'dambomo mpaka ku Giliyadi, panalibe mzinda wa malinga aatali ndi umodzi womwe umene udatikanika kugwetsa. Chauta adatithandiza kulanda mizinda yonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kuyambira ku Aroere, ndiko kumphepete kwa mtsinje wa Arinoni, ndi kumudzi wokhala kumtsinje kufikira ku Giliyadi, kunalibe mudzi wakutitalikira malinga ake; Yehova Mulungu wathu anapereka yonse pamaso pathu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kuchokera ku Aroeri mʼmphepete mwa mtsinje wa Arinoni ndi ku mzinda wa ku mtsinjeko mpaka kukafika ku Giliyadi, panalibe ndi mzinda ndi umodzi omwe umene unatikanika kuwugonjetsa. Yehova Mulungu wathu anatipatsa onsewo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kuyambira ku Aroeri, ndiko kumphepete kwa mtsinje wa Arinoni, ndi ku mudzi wokhala kumtsinje kufikira ku Gileadi, kunalibe mudzi wakutitalikira malinga ace; Yehova Mulungu wathu anapereka yonse pamaso pathu.