Deuteronomy 2:37 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma ku dziko la Aamoni sitidadzereko, ndiye kuti m'mbali mwa mtsinje wa Yaboki kapena kuti mizinda ya ku dziko lamapiri, kapenanso kwina kulikonse kumene Chauta, Mulungu wathu, adaatiletsa kupitako.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ku dziko la ana a Amoni lokha simunayandikiza; dera lonse la mtsinje wa Yaboki, ndi midzi ya kumapiri, ndi kwina kulikonse Yehova Mulungu wathu anatiletsa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Molingana ndi lamulo la Yehova Mulungu wathu, simunalowerere dziko lililonse la Aamoni, ngakhale dera lonse la ku mtsinje wa Yaboki kapena dera lozungulira dera la ku mizinda ya ku mapiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ku dziko la ana a Amoni lokha simunayandikiza; dera lonse la mtsinje wa Yaboki, ndi midzi ya kumapiri, ndi kwina kuli konse Yehova Mulungu wathu anatiletsa.