Deuteronomy 2:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta, Mulungu wanu, wakudalitsani pa ntchito zonse zimene mwachita. Wakusamalirani pa ulendo wanu m'chipululu chachikuluchi. Chauta, Mulungu wanu, wakhala nanu pa zaka makumi anai zonsezi, ndipo simudasoŵe kanthu kalikonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti Yehova Mulungu wanu anakudalitsani mu ntchito zonse za manja anu; anadziwa kuyenda kwanu m'chipululu ichi chachikulu; zaka izi makumi anai Yehova Mulungu wanu anakhala ndi inu; simunasowa kanthu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova Mulungu wanu wakudalitsani mʼntchito zonse za manja anu. Iye wakuyangʼanirani pa ulendo wanu wodutsa mʼchipululu chachikulu. Yehova Mulungu wanu wakhala nanu mʼzaka makumi anayi, ndipo simunasowe kalikonse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti Yehova Mulungu wanu anakudalitsani mu nchito zonse za manja anu; anadziwa kuyenda kwanu m'cipululu ici cacikuru; zaka izi makumi anai Yehova Mulungu wanu anakhala ndi inu; simunasowa kanthu.