Deuteronomy 2:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo Chauta adandiwuza kuti, “Musaŵavute Amowabu, zidzukulu za Loti. Musachite nawo nkhondo. Iwoŵa ndaŵapatsa dziko la Ari, ndipo sindikupatsani ngakhale gawo lomwe la dziko laolo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yehova anati kwa ine, Usavuta Mowabu, kapena kuutsana naye nkhondo; popeza sindidzakupatsako dziko lake likhale lakolako; pakuti ndinapatsa ana a Loti Ari likhale laolao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Yehova anati kwa ine, “Musawavutitse Amowabu kapena kuwaputa kuti muchite nawo nkhondo popeza sindidzakupatsani gawo lina lililonse la dziko lawo. Ndinapereka Ari kwa adzukulu a Loti ngati chuma chawo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo tinatembenuka ndi kudzera njira ya cipululu ca Moabu. Ndipo Yehova anati kwa ine, Usabvuta Moabu, kapena kuutsana naye nkhondo; popeza sindidzakupatsako dziko lace likhale lako lako; pakuti ndinapatsa ana a Loti Ari likhale lao lao.