Deuteronomy 20:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mukadzapita kukamenyana ndi adani anu, ngati muwona kuti magaleta ao ngochuluka kuposa anu, ngamira zao ndi zochulukanso, ndipo ngakhale ankhondo ao omwe ngokuposani, musakaŵaope. Chauta, Mulungu wanu, amene adakupulumutsani ku Ejipito, adzakhala nanu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamene mutuluka pa mdani wanu kunkhondo, ndi kuona akavalo ndi magaleta ndi anthu akuchulukira inu, musawaopa; popeza Yehova Mulungu wanu, amene anakukwezani kukutulutsani m'dziko la Ejipito, ali ndi inu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamene mukupita kokachita nkhondo ndi adani anu, mukaona akavalo kapena magaleta kapena gulu la ankhondo kuposa inuyo musamaope chifukwa Yehova Mulungu wanu, amene anakutulutsani ku Igupto adzakhala nanu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamene muturuka pa mdani wanu kunkhondo, ndi kuona akavalo ndi magareta ndi anthu akucurukira inu, musawaopa; popeza Yehova Mulungu wanu, amene anakukwezani kukuturutsani m'dziko la Aigupto, ali ndi inu.