Deuteronomy 20:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene muzinga mzinda nthaŵi yaitali ndi cholinga choti muulande, musagwetse mitengo yake yazipatso, mungathe kudya zipatso zake, koma mitengo yake musagwetse, chifukwa adani anu si mitengoyo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamene mumangira tsasa mudzi masiku ambiri, pouthirira nkhondo kuugwira, usamaononga mitengo yake ndi kuitema ndi nkhwangwa; pakuti ukadyeko, osailikha; pakuti mtengo wa m'munda ndiwo munthu kodi kuti uumangire tsasa?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mukalimbana ndi mzinda nthawi yayitali, kuchita nawo nkhondo pofuna kuwugonjetsa, musawononge podula mitengo yake ndi nkhwangwa, osayidula chifukwa zipatso zakezo mukhoza kudya. Kodi mitengo ya ku munda ndi anthu kuti mukalimbane nayo?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamene mumangira tsasa mudzi masiku ambiri, pouthirira nkhondo kuugwira, usamaononga mitengo yace ndi kuitema ndi nkhwangwa; pakuti ukadyeko, osailikha; pakuti mtengo wa m'munda ndiwo munthu kodi kuti uumangire tsasa?