Deuteronomy 20:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kodi alipo pano wina amene wangooka mipesa m'munda, koma osakhala ndi mwai woti nkuthyola mphesa zake? Ngati alipo abwerere kwao, mwinamwina akaphedwa pa nkhondo, ndiye kuti ndi wina amene adzamwe vinyoyo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndani munthuyo anaoka munda wamphesa osalawa zipatso zake? Amuke nabwerere kunyumba yake, kuti angafe kunkhondo, nangalawe munthu wina zipatso zake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kodi pali wina amene analima munda wamphesa ndipo sanayambe kudyerera? Ayambe wapita ku mudzi chifukwa mwina akafera ku nkhondo ndipo wina adzadyerera mundawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndani munthuyo ananka munda wamphesa osalawa zipatso zace? amuke nabwerere ku nyumba yace, kuti angafe kunkhondo, nangalawe munthu wina zipatso zace.