Deuteronomy 20:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kodi alipo wina pano amene adafunsira mbeta koma mkaziyo sanaloŵane naye? Ngati alipo, abwerere kwao, mwinamwina akaphedwa pa nkhondo, ndiye kuti ndi wina amene adzakwatire mbetayo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo munthuyo ndani anapala bwenzi ndi mkazi osamtenga? Amuke nabwerere kunyumba kwake, kuti angafe kunkhondo, nangamtenge munthu wina.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kodi pali amene wachita chinkhoswe ndi mkazi ndipo sanamukwatire mkaziyo? Ayambe wabwerera ku mudzi chifukwa mwina akafera ku nkhondo ndipo wina adzakwatira mkaziyo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo munthuyo ndani anapala bwenzi ndi mkazi osamtenga? amuke nabwerere kunyumba kwace, kuti angafe kunkhondo, nangamtenge munthu wina.