Deuteronomy 20:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo akuluakuluwo adzafunsanso anthu kuti, “Kodi alipo pano wina aliyense amene akuwopa ndipo mtima wake wafumuka ndi mantha? Ngati alipo, abwerere kwao, kuti angamakadederetse anzake.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo akapitao anenenso kwa anthu, ndi kuti, Munthuyo ndani wakuchita mantha ndi wofumuka mtima? Amuke nabwerere kunyumba kwake, ingasungunuke mitima ya abale ake monga mtima wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo akuluakulu ankhondowo akapitirize kuti, “Kodi pali amene akuchita mantha kapena kutaya mtima? Abwerere ku mudzi kuopa kuti abale ake angatayenso mtima.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo akapitao anenenso kwa anthu, ndi kuti, Munthuyo ndani wakucita mantha ndi wofumuka mtima? amuke nabwerere kunyumba kwace, ingasungunuke mitima ya abale ace monga mtima wace.