Deuteronomy 21:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake mutaona kuti simukumfunanso, mumleke, apite mwaufulu kumene akufuna. Simungathe kumuyesanso kapolo kapena kumgulitsa, chifukwa mudakhala naye malo amodzi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kudzali, mukapanda kukondwera naye, mumlole apite komwe afuna; koma musamgulitsa ndalama konse, musamamuyesa chuma, popeza wamchepetsa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngati simukukondweretsedwa naye, muloleni kuti apite kumene afuna. Musamugulitse kapena kumuzunza ngati kapolo, popeza mwamuchotsa ulemu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kudzali, mukapanda kukondwera naye, mumlole apite komwe afuna; koma musamgulitsa ndalama konse, musamamuyesa cuma, popeza wamcepetsa.