Deuteronomy 21:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mwana wake woyamba kubadwa uja ampatse moŵirikiza, ngakhale kuti ndi mwana amene mai wake ndi wokondedwa pang'ono. Munthu ayenera kuvomera mwana wake woyamba, ndi kumpatsa gawo limene lili lake potsata lamulo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma azivomereza wobadwa woyamba, mwana wa wodana naye, ndi kumwirikizira gawo lake la zake zonse; popeza iye ndiye chiyambi cha mphamvu yake; zoyenera woyamba kubadwa nzake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye ayenera kuonetsa kuti mwana wake wamwamuna wa mkazi wosakondedwayo ndiye woyamba kubadwa pomupatsa miyeso iwiri ya zonse zimene ali nazo. Mwana wamwamuna ameneyo ndiye chizindikiro cha mphamvu za abambo ake. Ufulu wokhala mwana wamwamuna woyamba ndi wake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma azibvomereza wobadwa woyamba, mwana wa wodana naye, ndi kumwirikizira gawo lace la zace zonse; popeza iye ndiye ciyambi ca mphamvu yace; zoyenera woyamba kubadwa nzace.