Deuteronomy 21:20 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Makolowo auze akuluakuluwo kuti, “Mwana wathu ndi wokanika ndipo ndi wachipongwe safuna kutimvera, ndi wadyera ndiponso chidakwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo anene kwa akulu a mudzi wake, Mwana wathu wamwamuna uyu ngwopulukira ndi wopikisana nafe, wosamvera mau athu, ndiye womwazamwaza, ndi woledzera.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
akawawuze akuluakuluwo kuti, “Mwana wathu wamwamunayu ndi wosamva ndi wowukira. Iyeyu satimvera. Ndi mwana wadyera komanso ndi chidakwa.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo anene kwa akulu a mudzi wace, Mwana wathu wamwamuna uyu ngwopulukira ndi wopikisana nafe, wosamvera mau athu, ndiye womwazamwaza, ndi woledzera.