Deuteronomy 21:23 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
mtembowo usagonere pamtengopo. Uikidwe tsiku lomwelo, chifukwa kuti mtembo ugonerere pamtengo ndi chinthu chobweretsa matemberero a Mulungu. Kwirirani mtembowo, kuwopa kuti mungaipitse dziko limene Chauta, Mulungu wanu, akukupatsanilo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
mtembo wake usakhale pamtengo usiku wonse, koma mumuike ndithu tsiku lomwelo; pakuti wopachikidwa pamtengo atembereredwa ndi Mulungu; kuti mungadetse dziko lanu limene Yehova Mulungu wanu akupatsani likhale cholowa chanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
musasiye mtembowo pa mtengopo usiku wonse. Muonetsetse kuti mwakawukwirira tsiku lomwelo, chifukwa aliyense wopachikidwa pamtengo ndi wotembereredwa ndi Mulungu. Musayipitse dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani ngati cholowa chanu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
mtembo wace usakhale pamtengo usiku wonse, koma mumuike ndithu tsiku lomwelo; pakuti wopacikidwa pamtengo atembereredwa ndi Mulungu; kuti mungadetse dziko lanu limene Yehova Mulungu wanu akupatsani likhale colowa canu.