Deuteronomy 21:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ansembe Achilevi apitekonso kumeneko, chifukwa ndiwo amene ayenera kumaweruza milandu yonse ya ndeu ndi ya kupha. Chauta, Mulungu wanu, wasankha iwowo kuti akhale atumiki ake, ndiponso kuti azidalitsa m'dzina lake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo ansembe, ana a Levi, ayandikize; pakuti Yehova Mulungu wanu anasankha iwo kumtumikira ndi kudalitsa m'dzina la Yehova; ndipo kutengana konse ndi kupandana konse kukonzeke monga mwa mau awa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ansembe, ana a Aaroni, adzapite patsogolo pangʼono, popeza ndiwo amene Yehova Mulungu wanu anawasankha kuti azitumikira, kupereka mdalitso mʼdzina la Yehova ndi kugamula milandu yonse yamikangano ndi yovulazana.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo ansembe, ana a Levi, ayandikize; pakuti Yehova Mulungu wanu anasankha iwo kumtumikira ndi kudalitsa m'dzina la Yehova; ndipo kutengana konse ndi kupandana konse kukonzeke monga mwa mau awa.