Deuteronomy 21:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono atsogoleri onse ochokera ku mudzi wa pafupi ndi pamene panali munthu wophedwayo, asambe m'manja pamwamba pa ng'ombe ija imene adaithyola khosi m'dambo muja.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo akulu onse a mudziwo wokhala pafupi pa munthu wophedwayo azisamba manja ao pa ng'ombeyo yodulidwa khosi m'chigwamo;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka akuluakulu a mzinda wapafupi kwambiri ndi mtembowo adzasamba mʼmanja pamwamba pa ngʼombe yothyoledwa khosi ija,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo akuru onse a mudziwo wokhala pafupi pa munthu wophedwayo azisamba manja ao pa msoti woudula khosi m'cigwamo;