Deuteronomy 21:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Inu Chauta, khululukirani anthu anu Aisraele amene mudaŵaombola. Tikhululukireni ndipo musaike pa ife tchimo la kupha munthu wosalakwayu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Landirani, Yehova, chotetezera anthu anu Israele, amene munawaombola, ndipo musalole mwazi wosachimwa ukhale pakati pa anthu anu Israele; ndipo adzawatetezera cha mwaziwo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova, landirani nsembe yopepesa ya anthu anu Aisraeli amene munawapulumutsa, ndipo muwakhululukire tchimo la kupha munthu wosalakwa.” Mukatero ndiye kuti adzapezeka kuti ndi osalakwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Landirani, Yehova, cotetezera anthu anu Israyeli, amene munawaombola, ndipo musalole mwazi wosacimwa ukhale pakati pa anthu anu Israyeli; ndipo adzawatetezera ca mwaziwo.