Deuteronomy 22:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mukaona ng'ombe kapena nkhosa ya Mwisraele mnzanu ikusokera, musailekerere. Itengeni, mukampatse mwiniwake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mukapenya ng'ombe kapena nkhosa ya mbale wako zilikusokera musamazilekerera, muzimbwezera mbale wanu ndithu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngati uwona ngʼombe kapena nkhosa ya mʼbale wako ikusochera, usayilekerere koma uyesetse kuyibwezera kwa iye.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mukapenya ng'ombe kapena nkhosa ya mbale wako zirikusokera musamazilekerera, muzimbwezera mbale wanu ndithu.