Deuteronomy 22:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zitatero, makolo a mkaziyo atenge zizindikiro zotsimikizira akuluakulu abwalo am'mudzimo kuti mwana waoyo adaali namwali wosadziŵa mwamuna ndithu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
pamenepo atate wa namwaliyo ndi mai wake azitenga ndi kutuluka nazo zizindikiro za unamwali wake wa namwaliyo, kunka nazo kwa akulu a mudzi kuchipata;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
zikatero abambo ndi amayi ake ayenera kubweretsa chitsimikizo chakuti anali namwali kwa akuluakulu a mzinda ku chipata.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
pamenepo atate wa namwaliyo ndi mai wace azitenga ndi kuturuka nazo zizindikilo za unamwali wace wa namwaliyo, kumka nazo kwa akuru a mudzi kucipata;