Deuteronomy 22:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo bambo wake wa mtsikanayo aŵauze abwalowo kuti, “Ndidalola mwana wanga wamkazi kuti akwatiwe ndi munthu uyu, koma tsopano akuti sakumufuna.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo atate wa namwaliyo azinena kwa akulu, Ndinampatsa munthuyu mwana wanga wamkazi akhale mkazi wake, koma amuda;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Abambo ake a mtsikanayo adzanene kwa akuluakuluwo kuti, “Ine ndinamupatsa munthu uyu mwana wanga wamkazi kuti amukwatire, koma sakumufunanso.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo atate wa namwaliyo azinena kwa akuru, Ndinampatsa munthuyu mwana wanga wamkazi akhale mkazi wace, koma amuda;