Deuteronomy 22:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Wamnamizira momchititsa manyazi kuti ati sadali namwali wosadziŵa mwamuna pomkwatira. Koma pano tili ndi umboni wotsimikizira kuti mwana wangayu adaali namwali wangwiro ndithu. Onani, zizindikiro zake ndi izi.” Apo adzaonetse chovala cha mkaziyo kwa akuluakuluwo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo, taonani, wamneneza zoutsa mbiri yamanyazi, ndi kuti, Sindinapeza zizindikiro za unamwali wake m'mwana wako wamkazi; koma si izi zizindikiro za unamwali wa mwana wanga wamkazi. Ndipo azifunyulula chovalacho pamaso pa akulu a mudziwo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsopano wamunyoza ndipo wanena kuti, ‘Ine sindinapeze kuti mwana wanu wamkaziyu ndi namwali.’ Koma tsopano onani chitsimikizo ichi cha unamwali wa mwana wanga wamkazi.” Kenaka makolo a mtsikanayo adzaonetse kansalu kwa akuluakulu aja,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo, taonani, wamneneza zoutsa mbiri yamanyazi, ndi kuti, Sindinapeza zizindikilo za unamwali wace in'mwana wako wamkazi; koma si izi zizindikilo za unamwali wa mwana wanga wamkazi. Ndipo azifunyulula cobvalaco pamaso pa akulu a mudziwo.