Deuteronomy 22:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake amlipitsenso masekeli asiliva makumi khumi, ndipo azipereke kwa bambo wa mtsikanayo. Alipe ndithu chifukwa choti adanyozetsa mnamwali Wachiisraele amene sadamdziŵeko mwamuna. Komanso adzakhalabe mkazi wake ndithu, ndipo pa moyo wake wonse sadzathanso kumsudzula.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndi kumlipitsa masekeli makumi okhaokha khumi a siliva, ndi kuipereka kwa atate wa namwaliyo, popeza anamveketsa dzina loipa namwali wa Israele, ndipo azikhala mkazi wake, sakhoza kumchotsa masiku ake onse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo adzamulipitse ndalama zasiliva zokwana 100 nazipereka kwa abambo a mtsikana, chifukwa munthu uyu wayipitsa dzina la mtsikana wa Chiisraeli. Ayenera kukhalabe mkazi wake ndipo asadzamuleke moyo wake wonse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndi kumlipitsa masekeli makumi okha okha khumi a siliva, ndi kuipereka kwa atate wa namwaliyo, popeza anamveketsa dzina loipa namwali wa Israyeli, ndipo azikhala mkazi wace, sakhoza kumcotsa masiku ace onse.