Deuteronomy 22:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma ngati mwiniwake kwao nkutali, kapena simumdziŵa, itengeni mupite nayo kwanu, muisunge komweko. Koma mwiniwake akabwera kudzaifunafuna, mumpatse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ngati mbale wanu sakhala pafupi ndi inu, kapena mukapanda kumdziwa, mubwere nayo kwanu kunyumba yanu, kuti ikhale kwanu, kufikira mbale wanu akaifuna, ndipo wambwezera iyo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngati mʼbale wakoyo sakhala pafupi kapena sukudziwa kuti ndi yandani, uyitengere ku nyumba kwako ndi kuyisamala mpaka mwini wake atayilondola ndipo umubwezere.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ngati mbale wanu sakhala pafupi ndi inu, kapena mukapanda kumdziwa, mubwere nayo kwanu ku nyumba yanu, kuti ikhale kwanu, kufikira mbale wanu akaifuna, ndipo wambwezera iyo.