Deuteronomy 22:21 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
pamenepo apite naye pakhomo pa bambo wake. Pomwepo amuna amumzindamo amuphe pakumponya miyala. Mtsikanayo wachita chinthu chochititsa manyazi pakati pa mtundu wathu wa Israele pochita zadama m'nyumba ya bambo wake. Motero mudzachotsa choipa pakati pa inu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
pamenepo azimtulutsa namwaliyo ku khomo la nyumba ya atate wake, ndipo amuna a mudzi wake azimponya miyala kuti afe; popeza anachita chopusa m'Israele, kuchita chigololo m'nyumba ya atate wake; chotero uzichotsa choipacho pakati panu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
iyeyu ayenera kumutengera pa khomo pa abambo ake pamene anthu a mu mzinda wake akamuphere ndi miyala. Iyeyo wachita chinthu chochititsa manyazi mu Israeli pochita chiwerewere akanali pa khomo pa abambo ake. Muyenera kuchotsa zoyipa pakati panu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
pamenepo azimturutsa namwaliyo ku khomo la nyumba ya atate wace, ndipo amuna a mudzi wace azimponya miyala kuti afe; popeza anacita copusa m'Israyeli, kucita cigololo m'nyumba ya atate wace; cotero uzicotsa coipaco pakati panu.