Deuteronomy 22:24 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Muŵatenge onsewo, mupite nawo kunja kwa mzinda, ndipo muŵaphe poŵaponya miyala. Mtsikanayo aphedwe chifukwa ngakhale anali m'mudzi, sadakuwe kuti anthu adzamthandize. Mwamunayo aphedwe chifukwa wachimwa ndi mtsikana wofunsidwa mbeta ndi mnzake. Motero mudzachotsa choipa pakati panu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
muziwatulutsa onse awiri kunka nao ku chipata cha mudzi uwo, ndi kuwaponya miyala kuti afe; namwaliyo popeza sanafuule angakhale anali m'mudzi; ndi mwamuna popeza anachepetsa mkazi wa mnansi wake; chotero muzichotsa choipacho pakati panu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
muwatengere awiriwo ku chipata cha mzinda ndi kuwapha ndi miyala. Aphedwe chifukwa mtsikanayo anali pafupi ndi anthu ndipo sanakuwe kuti ena amuthandize ndipo mwamunayo chifukwa anayipitsa mkazi wa mwini. Muyenera kuchotsa choyipa pakati panu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
muziwaturutsa onse awiri kumka nao ku cipata ca mudzi uwo, ndi kuwaponya miyala kuti afe; namwaliyo popeza sanapfuula angakhale anali m'mudzi; ndi mwamuna popeza anacepetsa mkazi wa mnansi wace; cotero muzicotsa coipaco pakati panu.