Deuteronomy 22:26 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mtsikanayo musamchite kanthu chifukwa choti sadachite tchimo loyenera kufa nalo. Mlandu umenewu ukufanafana ndi wakuti munthu aputa mnzake, namupha.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
koma namwaliyo musamamchitira kanthu; namwaliyo alibe tchimo loyenera imfa; pakuti mlandu uwu ukunga munthu waukira mnzake namupha;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mtsikanayo musamuchite chilichonse, palibe tchimo limene wachita loti ayenera kuphedwa. Mlandu uwu ufanana ndi wa munthu amene alimbana ndi kupha mnzake woyandikana naye,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
koma namwaliyo musamamcitira kanthu; namwaliyo alibe cimo loyenera imfa; pakuti mlandu uwu ukunga munthu waukira mnzace namupha;