Deuteronomy 22:29 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Munthuyo alipe bambo wake wa mtsikanayo mtengo wofunsira mbeta, ndiye kuti masekeli asiliva makumi asanu, ndipo amtenge kuti akhale mkazi wake chifukwa choti adamkakamiza kuchita naye chigololo. Tsono pa moyo wake wonse sangathenso kumsudzula.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
pamenepo mwamuna amene anagona naye azipatsa atate wake wa namwaliyo masekeli makumi asanu a siliva, ndipo azikhala mkazi wake; popeza anamchepetsa; sakhoza kumchotsa masiku ake onse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
ayenera kuwalipira abambo ake a namwaliyo ndalama za siliva makumi asanu. Iye ayenera kumukwatira mkaziyo chifukwa wamuyipitsa, ndipo sadzamulekanso moyo wake wonse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
pamenepo mwamuna amene anagona naye azipatsa atate wace wa namwaliyo masekeli makumi asanu a siliva, ndipo azikhala mkazi wace; popeza anamcepetsa; sakhoza kumcotsa masiku ace onse.