Deuteronomy 22:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Bulu wa Mwisraele mnzanu akagona mu mseu, muutseni. Muchitenso chimodzimodzi ndi ng'ombe yake, musailekerere. Mthandizeni mnzanu kuti adzutse choŵetacho.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mukapenya bulu kapena ng'ombe ya mbale wanu, zitagwa m'njira, musamazilekerera; mumthandize ndithu kuziutsanso.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngati wapeza bulu kapena ngʼombe ya mʼbale wako itagwa panjira, usayilekerere. Ithandize kuti idzuke.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mukapenya buru kapena ng'ombe ya mbale wanu, zitagwa m'njira, musamazilekerera; mumthandize ndithu kuziutsanso.