Deuteronomy 22:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Akazi asamavale zovala za amuna, chimodzimodzi amuna asamavale zovala za akazi. Chauta, Mulungu wanu, amanyansidwa nawo anthu ochita zotere.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mkazi asavale chovala cha mwamuna, kapena mwamuna asavale chovala cha mkazi; pakuti aliyense wakuchita izi Yehova Mulungu wanu anyansidwa naye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Akazi asavale zovala za amuna, kapena mwamuna kuvala zovala za akazi, pakuti Yehova Mulungu wanu amanyansidwa ndi aliyense wochita izi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mkazi asabvale cobvala ca mwa muna, kapena mwamuna asabvale cobvala ca mkazi; pakuti ali yense wakucita izi Yehova Mulungu wanu anyansidwa naye.