Deuteronomy 23:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ngati mwamana aliyense pakati panu waipitsidwa chifukwa chakuti wadzilotera usiku, atuluke m'zithando ndipo akhale kunja kwa zithandozo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakakhala munthu pakati pa inu, ndiye wosayera chifukwa chochitika usiku, azituluka kunja kwa chigono, asalowe pakati pa chigono;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Wina mwa asilikali anu akadziwonongera ndi umuna usiku, ayenera kuchoka pa msasapo ndipo akhale kunja kwa msasa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakakhala munthu pakati pa inu, ndiye wosayera cifukwa cocitika usiku, azituruka kunja kwa cigono, asalowe pakati pa cigono;