Deuteronomy 23:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zithando zanuzo zizikhala zaukhondo, chifukwa Chauta, Mulungu wanu, amayenda pakati pa zithando zanu, kuti akutchinjirizeni ndi kukupambanitsani kwa adani anu. Choncho m'zithando zanu mukhale mwabwino, kuti Chauta asaone kanthu kalikonse konyansa ndi kukufulatirani.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
popeza Yehova Mulungu wanu ayenda pakati pa chigono chanu kukupulumutsani ndi kupereka adani anu pamaso panu; chifukwa chake chigono chanu chikhale chopatulika; kuti angaone kanthu kodetsa mwa inu, ndi kukupotolokerani.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti Yehova Mulungu wanu amayendayenda ku msasa wanu kukutchinjirizani ndi kupereka adani anu kwa inu. Nʼchifukwa chake msasa wanu uzikhala wopatulika kuti mwina angaone china chonyansa nabwerera osakuyandikirani.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
popeza Yehova Mulungu wanu ayenda pakati pa cigono canu, kukupulumutsani ndi kupereka adani anu pamaso panu; cifukwa cace cigono canu cikhale copatulika; kuti angaone kanthu kodetsa mwa inu, ndi kukupotolokerani.