Deuteronomy 23:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndalama zozipeza mwa njira yadama yotereyi, yochitika ndi mkazi kapena mwamuna, musabwere nazo ku Nyumba ya Chauta, Mulungu wanu, kuti mukwaniritsire malonjezo anu, poti zimenezi Chauta, Mulungu wanu, amadana nazo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Musamabwera nayo mphotho ya wachigololo, kapena mtengo wake wa galu kulowa nazo m'nyumba ya Yehova Mulungu wanu, chifukwa cha chowinda chilichonse; pakuti onse awiriwa Yehova Mulungu wanu anyansidwa nao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Musabweretse malipiro a wachiwerewere wamkazi kapena wamwamuna Mʼnyumba ya Yehova Mulungu wanu kudzapereka za malumbiro aliwonse, chifukwa Yehova Mulungu wanu amadana ndi zimenezi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Musamabwera nayo mphotho ya wacigololo, kapena mtengo wace wa garu kulowa nazo m'nyumba ya Yehova Mulungu wanu, cifukwa ca cowinda ciri conse; pakuti onse awiriwa Yehova Mulungu wanu anyansidwa nao.